18 “Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa anthu osauka. Anandituma kudzalengeza za ufulu kwa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina komanso zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale pa ufulu,+