6 Choncho Yesu ananyamuka nawo limodzi. Koma atatsala pangʼono kufika kunyumbako, anakumana ndi anzake a mtsogoleri wa asilikali uja, amene anawatuma kuti adzamuuze kuti: “Ambuye musavutike ndi kubwera, sindine munthu woyenera kuti mulowe mʼnyumba mwanga.+