12 Atayandikira pageti la mzindawo, anakumana ndi anthu atanyamula maliro. Munthu amene anamwalirayo anali mwana wamwamuna yekhayo kwa mayi ake.+ Komanso mayi akewo anali mkazi wamasiye. Gulu lalikulu ndithu la anthu ochokera mumzindawo linali limodzi ndi mayiwo.