22 Choncho poyankha anauza amuna awiri aja kuti: “Pitani mukauze Yohane zimene mwaona ndi kumva: Amene anali ndi vuto losaona akuona,+ olumala akuyenda, akhate akuyeretsedwa ndipo amene anali ndi vuto losamva akumva.+ Akufa akuukitsidwa ndipo osauka akuuzidwa uthenga wabwino.+