-
Luka 14:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Kenako anauzanso munthu amene anamuitana uja kuti: “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usaitane anzako, kapena azichimwene ako, kapena achibale ako, kapena anthu olemera omwe amakhala nawe pafupi. Mwina nthawi ina iwonso angadzakuitane ndipo adzakhala ngati akukubwezera.
-