27 Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka, koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chimabweretsa moyo wosatha.+ Mwana wa munthu adzakupatsani chakudya chimenechi chifukwa Atate, Mulungu yekhayo, waika chidindo chake pa iye chomuvomereza.”+