35 Mose yemweyo, amene iwo anamukana nʼkunena kuti, ‘Ndani anakupatsa udindo woti uzitilamulira komanso kutiweruza?’+ ndi amene Mulungu anamutumiza+ ngati wolamulira ndi mpulumutsi kudzera mwa mngelo amene anaonekera kwa iye pachitsamba chaminga chija.