45 Makolo athu analandira chihemachi kwa makolo awo ndipo analowa nacho limodzi ndi Yoswa mʼdziko limene munali anthu a mitundu ina.+ Anthu amenewa Mulungu anawathamangitsa pamaso pa makolo athu+ ndipo chihemacho chinakhala mʼdzikoli mpaka nthawi ya Davide.