11 Tsopano tamvera! Dzanja la Yehova lili pa iwe ndipo ukhala wakhungu. Kwakanthawi, suthanso kuona kuwala kwa dzuwa.” Nthawi yomweyo anaona nkhungu yamphamvu mʼmaso mwake ndiponso mdima wandiweyani, ndipo anayamba kufufuza anthu oti amugwire dzanja ndi kumutsogolera.