21 Koma musalole kuti akunyengerereni, chifukwa amuna oposa 40 akufuna kudzamudikirira panjira. Anthu amenewa alumbira mochita kudzitemberera kuti saadya kapena kumwa chilichonse mpaka atamupha.+ Moti panopa akonzeka, akungoyembekezera chilolezo chanu.”