18 Abulahamu anali ndi chiyembekezo ndiponso chikhulupiriro chakuti adzakhala bambo wa mitundu yambiri, ngakhale kuti zimenezi zinkaoneka kuti nʼzosatheka. Anakhulupirira zimenezi mogwirizana ndi zimene zinanenedwa kuti: “Umu ndi mmene mbadwa zako zidzakhalire.”+