25 Chifukwa sindikufuna kuti mukhale osadziwa abale za chinsinsi chopatulika chimenechi,+ kuopera kuti mungadzione ngati anzeru. Chinsinsicho nʼchakuti ena mu Isiraeli aumitsa mitima yawo mpaka chiwerengero chonse cha anthu ochokera mʼmitundu ina chitakwanira.