18 Tonsefe tili ndi nkhope zosaphimba ndipo tili ngati magalasi amene amaonetsa ulemerero wa Yehova. Tikamaonetsa ulemererowu, timasintha nʼkukhala ngati chifaniziro chake ndipo timaonetsa ulemerero wowonjezerekawonjezereka mofanana ndendende ndi mmene Yehova, amene ndi Mzimu, watisinthira.+