4 Chifukwa wina akabwera kwa inu nʼkulalikira za Yesu wosiyana ndi amene tinamulalikira, kapena akakubweretserani mzimu wosiyana ndi umene munalandira kale, kapena uthenga wabwino wosiyana ndi umene munaulandira,+ inu mumangomulandira munthu woteroyo.