23 Kapena kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankha ngati wamisala, ineyo ndiye mtumiki wa Khristu woposa iwowo. Ndachita zambiri kuposa iwowo,+ ndinamangidwa kambirimbiri,+ ndinamenyedwa kosawerengeka ndipo ndinabwererapo lokumbakumba kambirimbiri.+