26 Ndinayenda maulendo ambirimbiri, ndinakumana ndi zoopsa mʼmitsinje komanso ndinakumana ndi achifwamba pamsewu. Ndinakumananso ndi zoopsa kuchokera kwa anthu a mtundu wanga,+ anthu a mitundu ina,+ mumzinda,+ mʼchipululu, panyanja ndi pakati pa abale achinyengo.