14 Ndine wokonzeka kubwera kwa inu ndipo kano ndi kachitatu kukhala wokonzeka. Koma sindidzakhala katundu wolemetsa chifukwa sindikufuna zinthu zanu,+ koma inuyo. Paja si udindo wa ana+ kusunga chuma kuti chidzathandize makolo awo, koma makolo ndi amene ayenera kusungira chuma ana awo.