21 Mwina ndikadzabweranso, Mulungu wanga adzalola kuti ndichite manyazi pamaso panu. Ndipo mwina ndidzalirira anthu ambiri amene anachimwa koma sanalape pa khalidwe lawo lonyansa, chiwerewere ndiponso khalidwe lawo lopanda manyazi limene akhala akuchita.