17 Komanso ineyo ndikuti: Choyamba, Mulungu anachita pangano ndi Abulahamu ndipo patapita zaka 430+ anapereka Chilamulo kwa anthu ake. Koma Chilamulocho sichinathetse pangano ndi lonjezo limene Mulungu anachita ndi Abulahamu, kuti lonjezolo lisagwirenso ntchito.