18 Musalole kuti munthu aliyense amene amasangalala ndi kudzichepetsa kwachinyengo komanso kulambira angelo akulepheretseni kudzalandira mphoto.+ “Munthu woteroyo amaumirira” zinthu zimene waona ndipo maganizo ake ochimwa amamuchititsa kuti azidzitukumula popanda chifukwa chomveka.