6 Koma Timoteyo wangofika kumene kuno kuchokera kumeneko+ ndipo watiuza nkhani yabwino yokhudza kukhulupirika kwanu ndi chikondi chanu. Watiuza kuti mukupitiriza kutikumbukira ndipo mumatikonda komanso kuti mukulakalaka kutiona ngati mmene ifenso tikulakalakira kukuonani.