2 musalole kuti wina aliyense asinthe maganizo anu omwe ndi olondola. Musasokonezeke ngati wina atanena kuti tsiku la Yehova+ lafika, ngakhale atanena kuti uthengawo ndi wochokera kwa Mulungu,+ kapena atanena kuti anawerenga mʼkalata imene anthu ena akunena kuti ife ndi amene tinalemba.