3 Iye amasonyeza bwino ulemerero wa Mulungu+ ndipo ndi chithunzi chenicheni cha Mulunguyo.+ Komanso mawu ake amphamvu amathandiza kuti zinthu zikhalepobe. Ndipo atatiyeretsa potichotsera machimo athu,+ anakhala kudzanja lamanja la Wolemekezeka kumwamba.+