25 Samalani kuti musasiye kumumvera amene akulankhulayo. Chifukwa ngati omwe anakana kumvera amene anapereka chenjezo la Mulungu padziko lapansi sanapulumuke, ndiye kuli bwanji ifeyo? Nafenso sitidzapulumuka tikapanda kumvera amene amalankhula ali kumwamba.+