4 Kudzera mʼzinthu zimenezi, iye watilonjeza zinthu zamtengo wapatali ndi zazikulu kwambiri,+ kuti mogwirizana ndi malonjezo amenewa mukhale ndi ulemerero umene Mulungu ali nawo.+ Wachita zimenezi chifukwa tinasiya kuchita makhalidwe oipa amʼdzikoli amene amayamba chifukwa cholakalaka zinthu zoipa.