16 Pamene tinkakudziwitsani za mphamvu za Ambuye wathu Yesu Khristu komanso zokhudza kukhalapo kwake, sitinatengere nkhani zabodza zimene anthu amapeka mochenjera. Koma tinakuuzani zinthu zokhudza ulemerero wake zimene tinachita kuona ndi maso athu.+