19 Nʼchifukwa chake sitikayikira ngakhale pangʼono kuti mawu aulosiwa adzakwaniritsidwa ndipo mukuchita bwino kuwaganizira mozama. Mawu amenewa aziwala mʼmitima yanu ngati nyale+ imene ikuwala mumdima. Pitirizani kuchita zimenezi mpaka mʼbandakucha, nthanda+ itatuluka.