20 Ndithudi, ngati anapulumuka ku zodetsa za dzikoli+ chifukwa chodziwa molondola Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, koma nʼkuyambiranso kuchita zinthu zomwe zija mpaka kugonjetsedwa nazo, makhalidwe awo amakhala oipa kwambiri kuposa poyamba.+