12 Muzichita zimenezi pamene mukuyembekezera komanso kukumbukira nthawi zonse kubwera kwa tsiku la Yehova.+ Pa tsikuli kumwamba kudzapsa ndi moto nʼkuwonongekeratu+ ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri nʼkusungunuka.