10 Munthu amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu amavomereza mumtima mwake umboni umene Mulungu wamupatsa. Munthu amene sakhulupirira Mulungu amamupangitsa kuoneka ngati wabodza,+ chifukwa sakhulupirira umboni umene Mulungu anapereka wokhudza Mwana wake.