10 Nʼchifukwa chake ndikadzabwera, ndidzaulula zimene akuchita pofalitsa mabodza onena za ife.+ Ndipo chifukwa chosakhutira ndi zimenezi, amakana kulandira abale+ mwaulemu. Komanso anthu amene amafuna kuwalandira, amayesa kuwatsekereza ndiponso kuwachotsa mumpingo.