24 Komabe, ena nonse amene muli ku Tiyatira, nonsenu amene simutsatira chiphunzitso chimenechi, amene simukudziwa chilichonse chokhudza zinthu zimene amati ndi “zinthu zozama za Satana,”+ ndikukuuzani kuti: Sindikusenzetsani katundu aliyense wolemera.