6 Mboni zimenezi zili ndi mphamvu yotseka kumwamba+ kuti mvula isagwe+ mʼmasiku onse amene zikunenera. Zilinso ndi mphamvu yosandutsa madzi kuti akhale magazi+ komanso yobweretsa mliri wamtundu uliwonse padziko lapansi maulendo ambirimbiri mmene zikufunira.