3 Iye wamwetsa mitundu yonse ya anthu vinyo wa chilakolako chake cha chiwerewere.+ Ndipo mafumu a dziko lapansi anachita naye chiwerewere.+ Amalonda apadziko lapansi analemera chifukwa cha zinthu zambiri zamtengo wapatali zimene mkazi ameneyu anadziunjikira mopanda manyazi.”