19 Iwo anathira fumbi pamitu pawo akufuula, kulira ndi kumva chisoni, ndipo anati: ‘Nʼzomvetsa chisoni kuti zimenezi zachitikira mzinda waukuluwu. Anthu onse amene anali ndi ngalawa panyanja analemera chifukwa cha chuma chake. Zatheka bwanji kuti mzindawu uwonongedwe mu ola limodzi.’+