-
Genesis 30:40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
40 Kenako, Yakobo anachotsapo nkhosa zamphongo zing’onozing’ono n’kuziika pazokha. Atatero, anapatula nkhosa zonse zamizeremizere ndi zofiirira zimene zinali pakati pa ziweto za Labani. Kenako anatembenuza nkhosa zotsalazo kuti ziyang’ane zamizeremizere ndi zofiirira zija. Iye anaika ziweto zake pazokha, ndipo sanaziphatikize ndi ziweto za Labani.
-