28 Kenako wansembe azipaka ena mwa mafuta amene ali pachikhatho chake m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu chakumwendo wa kudzanja lamanja pamene anam’paka magazi a nsembe ya kupalamula.+