15 “Kenako azipha mbuzi ya nsembe yamachimo yoperekera anthuwo,+ n’kulowa ndi magazi ake kuchipinda, kuseri kwa nsalu yotchinga.+ Kumeneko magaziwo+ azichita nawo zimene anachita ndi magazi a ng’ombe yamphongo ija. Azidontheza magaziwo patsogolo pa chivundikiro.