21 Ndipo Aroni aziika manja ake onse+ pamutu pa mbuziyo ndi kuvomereza+ zolakwa zonse+ za ana a Isiraeli ndiponso kusamvera kwawo m’machimo awo onse.+ Zonsezi aziziika pamutu pa mbuzi ija+ ndi kuipereka kwa munthu amene am’sankhiratu+ kuti akaisiye kuchipululu.+