14 Koma mwamuna wake akhoza kukhala ndi nsanje+ mumtima mwake, n’kumaganiza kuti mkaziyo sanayende bwino, pamene mkaziyo wadziipitsadi. Kapena mwamuna akhoza kukhala ndi nsanje mumtima mwake n’kumaganiza kuti mkazi wake sanayende bwino, pamene mkaziyo sanadziipitse.