-
Numeri 5:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Mulimonsemo, mwamunayo azitenga mkaziyo n’kupita naye kwa wansembe.+ Azipita ndi nsembe ya mkaziyo ya ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Ufawo asamauthire mafuta kapena lubani,*+ chifukwa ndi nsembe yambewu yansanje, nsembe yambewu yachikumbutso, yokumbutsa cholakwa.
-