54 Choncho Mose ndi wansembe Eleazara analandira zinthu zagolidezo kwa atsogoleri a magulu a asilikali 1,000, ndiponso kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100. Ndipo zinthu zagolidezo anakaziika m’chihema chokumanako, kuti zikhale chikumbutso+ kwa ana a Isiraeli pamaso pa Yehova.