4 Komabe, Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Anthu amene atsalawa ndi ochulukabe.+ Pita nawo kumadzi kuti ndikawayese kumeneko. Ndiyeno amene ndidzakuuza kuti, ‘Uyu apite nawe,’ ameneyo apite nawe, koma aliyense amene ndidzakuuza kuti, ‘Uyu asapite nawe,’ ameneyo asapite nawe.”