15 Tsopano Alevi+ anatsitsa likasa la Yehova, pamodzi ndi bokosi lina lija mmene munali zinthu zagolide, n’kuliika pamwala waukulu uja. Kenako amuna a ku Beti-semesi+ anapereka nsembe zopsereza, ndipo anapitiriza kupereka nsembe kwa Yehova tsiku limenelo.