8 Kenako mutu wa Isi-boseti+ uja anafika nawo kwa Davide ku Heburoni ndi kuuza mfumuyo kuti: “Nawu mutu wa Isi-boseti mwana wa mdani wanu Sauli,+ amene anali kufunafuna moyo wanu.+ Lero Yehova wabwezera+ Sauli ndi mbadwa zake chifukwa cha inu mbuyanga mfumu.”