24 Pomaliza pake, iwo anabwera kudzapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina. Yehu anaika amuna 80 panja oti amuthandize ndipo anawauza kuti: “Aliyense amene athawitse munthu pa anthu amene ndikuwapereka m’manja mwanu, moyo wake ulowa m’malo mwa munthuyo.”+