31 Mfumuyo inaimirirabe pamalo ake+ ndipo inachita pangano+ pamaso pa Yehova, kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo+ ake ndi maumboni+ ake. Inanenanso kuti idzachita+ zimenezi ndi mtima wake wonse+ ndi moyo wake wonse,+ mogwirizana ndi mawu a pangano olembedwa m’bukulo.+