6 Tsopano Ezara anachoka panyumba ya Mulungu woona n’kupita kuchipinda chodyera+ cha Yehohanani mwana wa Eliyasibu. Ngakhale kuti anapita kumeneko, sanadye mkate+ kapena kumwa madzi, chifukwa anali kumva chisoni+ ndi kusakhulupirika kwa anthu ochokera ku ukapolo aja.