9 Choncho amuna onse a fuko la Yuda ndi la Benjamini anasonkhana ku Yerusalemu m’masiku atatu, ndipo umu munali m’mwezi wa 9,+ pa tsiku la 20 la mweziwo. Anthu onsewo anakhala pabwalo la nyumba ya Mulungu woona, akunjenjemera poganizira nkhaniyo komanso chifukwa kunali kugwa mvula yamvumbi.+