22 Woyang’anira+ Alevi pa ntchito ya panyumba ya Mulungu woona mu Yerusalemu anali Uzi mwana wa Bani. Bani anali mwana wa Hasabiya, Hasabiya anali mwana wa Mataniya,+ Mataniya anali mwana wa Mika+ wa m’banja la Asafu.+ A m’banja la Asafu anali oimba.+